Wednesday, January 17, 2007

Ndakatulo youkira

IMFA

Usachite matama imfa

Thakati ndiwe
Opanda chisoni
Polodza akulu

Ndiwedi mbanda
Mantha ulibe
Wamayi moyo pokhwathula

Yosamva mankhwala
Nthenda ndiwe
kuli chete ana watengera

Kwanthawi ndakusaka
Ndikakupeza
ndikupha

Usachite matama imfa.

No comments: